Tribal Race

T-No

0 fans

T-No


4:09
#1

 The easy, fast & fun way to learn how to sing: 30DaySinger.com

Zaka zikwi zangodutsa Yesu atawonekera
Mtundu wa Banthu wabadwa ufumu wake Maravi
Anachokera ku Congo nkuzafikira ku nkhondo
A Chewa ndi Akafula kulimbirana malowo
Moto moto umabuka akamasema zitsulo
Nkomwe dzina la Malawi inachokeratu ilo
Anali mphepete mwa nyanja
Kenako natchedwa a Nyanja
Anzawo ena Amang'anja
Anafika Atumbuka atadza
Angonde ndi Anyakyusa anachokera ku mpoto
Nkukhazikika ku Karonga kumpoto konko
1819 Angoni ndi Shaka Zulu
Analimbana, Ngoni nagonja kuthawako kwa a Zulu
1840 Jumbe wafika ku Nkhotakota
A Yao nagulitsa akapolo nkuwatumiza ku border
Inkosi Mbelwa nkunzagonjetsa Chikulamayembe
Angoni nalamula Atumbuka iwo mphavu alibe
1861, David Livingstone wafika
Kuzathetsa ukapolo ndi ma mission atayambika
Anayesetsa kuyankhulitsana ndi Jumbe, zinakanika
Ukapolo udapitilirabe a Yao adalimbika
1870 a Yao ambiri adatsata Chisilamu
Chifukwa chotengeka ndi anzawo ogulitsa akapolo
Ma Scottish missionary adafika Blantyre 1876
Nkukopa akapolo amene amatengedwa ndi Apwitikizi
Anayambapo kulalikira ndi kuphunzitsa muchi Nyanja
Kuti afikire ambiri popeza chinatchuka ndi chi Nyanja
A Tumbuka anachilandira chiphunzitso cha ma missionary mwansanga
Nawo ma missionary anayamba kuphunzitsa muchitumbuka
A Tonga ndi a Tumbuka anapulumuka kwa Angoni
Ataphunzira kwa ma missionary napeza nzeru zoposa Ngoni
1891 British protectorate inakhazikisidwa
Kugulitsa akapolo kunja kunathetsedwa
1893 ikungotukukano skulu
1895 kunatulukira a Nguru
Anali mtundu wodabwitsa kuchokera ku Mozambique
Analolera kugwira ntchito kwa Nzungu opanda ndalama zambiri
1904 a tsamunda anabweretsa thangata
A Mang'anja,  Nguru, a Sena ndi a Lomwe anagwira njakata
Analima malo ambiri, kupatsidwa malo ochepa
Anagwira ntchito kwambiri
Koma olemera ali ena
1915 Chilembwe anawukira
Nayimilira nkuwatsogoza anthu osasangalatsidwa
Adagonja, tsamunda atabwenza moto naye nkulusa
Anthu ambiri anaphedwa anathana ndi aliyense wotsutsa
1918 a Malawi amafuna chiyankhulo chimodzi
A govenor anakana chifukwa amadana ndi umodzi
A Tonga anagwirizana nkugwira zochititsa kaso
A Tumbuka ndi a Ngoni, nawonso anawukanso
1933 Livingstonia inakana chi Nyanja
Angoni nawo anachikana amati sichimawayanja
Chitumbuka chinasanduka chiyankhulo chovomelezeka
Pamodzi ndi chi Nyanja, ziwirizi zinavomelezedwa
1943 dzina la Anguru inafufutidwa
Analisintha, nkuyika Lomwe ponse pomwe limatchulidwa
Akachenjede odana ndi atsamunda anabwera pamodzi
1944 anagwirizana anapanga chipani chimodzi
1958 Kamuzu Banda anabwelera
Nawina support ya anthu ndi MCP atayimenyelera
1964, Federation inagwa
Nyasaland idapeza ufulu wodzilamulira yokha
A Malawi okha okha adakangana mu cabinet crisis
Kuwonetsa kuti panali ntchitobe nkatinkati mwachpanichi
Chitumbuka anachiletsa, chichewa kuvomeleza
Mpamene udani udapitilira nankera osalekeza
It's a race that we started
Tribalism is building a wall
We were one race united
But our difference divided us all
It's a race that we started
Tribalism is building a wall
Nkhondo, nkhondo
Kusiyanasiyanatuku kwayambitsa mpikisano

 Watch: New Singing Lesson Videos Can Make Anyone A Great Singer

Written by: Edward Chikhwenda

Lyrics © DistroKid

Lyrics Licensed & Provided by LyricFind

Discuss the Tribal Race Lyrics with the community:

0 Comments

    Citation

    Use the citation below to add these lyrics to your bibliography:

    Style:MLAChicagoAPA

    "Tribal Race Lyrics." Lyrics.com. STANDS4 LLC, 2024. Web. 28 Apr. 2024. <https://www.lyrics.com/lyric-lf/7465334/T-No/Tribal+Race>.

    Missing lyrics by T-No?

    Know any other songs by T-No? Don't keep it to yourself!

    Browse Lyrics.com

    Quiz

    Are you a music master?

    »
    Who co-wrote and performs the pop hit Fight Song?
    A Rachel Platten
    B Olivia
    C Ariana Grande
    D Billie Eilish

    Free, no signup required:

    Add to Chrome

    Get instant explanation for any lyrics that hits you anywhere on the web!

    Free, no signup required:

    Add to Firefox

    Get instant explanation for any acronym or abbreviation that hits you anywhere on the web!

    T-No tracks

    On Radio Right Now

    Loading...

    Powered by OnRad.io


    Think you know music? Test your MusicIQ here!